Kishore Kumar Hits

Lawi - Timalira lyrics

Artist: Lawi

album: Sunset in the Sky


Kodi wanyonga ndiye uti
Osakumana ndi mikwingwirima
Njira yomwe onse amoyo
Ayesedwa kulimba mtima
Zochititsa mantha ena
Zilimbitsa mtima ena
Tifanana ndikusiyana muzotipangitsa kulira
Timalira mu mtima
Mong'ung'udza ndi modandaula
Ululu ukasefukira timaliraso mwa mkuwe
Kulira kulibe mulingo
Champweteka ndiye ayamba
Sikuona nkhope kulira mayi maso ndiye mboni
Tose timalira
Zikawawa tikakhumudwa zikalemera zikachuluka
Mutu ukakula usale wamkomya (Mayo)
Timalira zikawawa tikakhumudwa zikalemera zikachuluka
Mutu ukakula usale wamkomya (Mayo)
Timalira mumtima timalira monga ana
Ndimisozi nayo imakhala ikulakatika
Timalira mumtima
Mayo
Nthawi zina ndimalira
Ndikakumbuka zowawa zimene ndaziona ine m'moyo
Moyo ndichonchobe basi
Mtima ulinayo misozi
Yoseoneka yongothera mkati
Ndimisozi yosapuputika amayo!!
Ooh ooh ooh
Ooh weh tsamba langa
Kuwala mudzuwa gwelera mumphepo
Kukongola kwako kosiliritsa kuli kunja
Ulira mkati
Oooh weh tsamba langa
Lira mumphepo asazindikire
Dziko likonda wolimba mtima mwana wanga
Tose timalira
Zikawawa tikakhumudwa zikalemera zikachuluka
Mutu ukakula usale wamkomya (Mayo)
Timalira zikawawa tikakhumudwa zikalemera zikachuluka
Mutu ukakula usale wamkomya (Mayo)
Timalira mumtima timalira monga ana
Ndimisozi nayo imakhala ikulakatika
Timalira mumtima

Поcмотреть все песни артиста

Other albums by the artist

Similar artists