Kishore Kumar Hits

Eli Njuchi - Ma Ine lyrics

Artist: Eli Njuchi

album: The Book of Eli


Anandikonda munthene ndisanabadwe
Amkayimba tinyimbo mwanawe utonthole
Anali pompa nsanayimilire
Anandikwawitsa anandiphuzitsa kuyenda
Nkhope yanu sindingayiwale
Ngayiwale ngayiwale nono
Ntchito zanu ndiwulure
Ndiwulure ndiwulure (lure)
Amayi anga sindingawanyoze
Ndili moyo sangamavutike
Kachala kanga sindingawatoze
Malipiro sindingawamalize
Amayi anga sindingawasale
Kuchepa komko tikanyemelane
Cha m'ma four phee tilangizane
Malipiro sindingawamalize
Musadabwe khalidwe ndinabela ma ine
Kuyankhula maonekedwe kaoneni ma ine
Musadabwe thanzilo
Ndili ndi mdalitso
Palowapo thandizo, zosezo zigwere
Ma ine, Ma ine
Ndisaname timamvana ndisaname timamva!
Ma ine, Ma ine
Tidzayimba jabulani tidzayimba jabula!
Nzoyamwira kuti ukhale mfumu mkoyambira
Ooh nanji ndidwale ndipomwe muwadiwire
Ooh oh maso awo
Ukawaona muli njira zawo
Muli masophenya mwana wawo
Kuti zitheke nditengepo gawo
Ooh ndipo zithuzi zawo
Atandifungatira m'manja mwawo
Zimawulura za mkati mwawo
Muli chikondi mtimwa mwawo
Musadabwe khalidwe ndinabela ma ine
Kuyankhula maonekedwe kaoneni ma ine
Musadabwe thanzilo
Ndili ndi mdalitso
Palowapo thandizo, zosezo zigwere
Ma ine, Ma ine
Ndisaname timamvana ndisaname timamva!
Ma ine, Ma ine
Tidzayimba jabulani tidzayimba jabula!
Ma ine, Ma ine
Ndisaname timamvana ndisaname timamva!
Ma ine, Ma ine
Tidzayimba jabulani tidzayimba jabulaaa!
Njuchi

Поcмотреть все песни артиста

Other albums by the artist

Similar artists