Kishore Kumar Hits

Lucius Banda - Palibe lyrics

Artist: Lucius Banda

album: LOVE & HATE (The 20th and Final Release)


This is ionine Soldier, Lucius Banda
Standing shoulder to shoulder
With Coss Chiwalo
Back home
Ufalitsi ndi wokhometsa misonkho
Adapita kukapemphera
Adalikunga pemphero mfalitsi
Lodzitamandila pamaso pa Yahweh
Wokhometsa nsonkho adangoyima
Paka corner kudzimvela chisoni
Pemphero lake lidali lalifupi
Ambuye khululukireni ochimwa ine
Tagundika tuthandiza wosowa
Komatu ndiye zachifalitsi
Katundu wake okwana mu jumbo
Koma pa social media photo mbwe mbwe mbwe
Amanyoza omwe achita zanzeru
Akuti iwo ndiye abwino
Sadziwa anzawo atsatira malemba
Chaku manja chakumanzere chisaone

Tikadzitchula kuti ndife abwino
Tidzinyenga chabe
Tikadziona ndife alunga-lunga
Tingopusa chabe
Poti wabwino ndi Mulungu yekha
Wosachimwa kose
Mavuto onse tipereke kwa iye
Iye wotilenga
Ndikuti palibe
Palibe munthu wopanda tchimo
Dziko lapansi ndi lochimwa
Adatitsoka mtunda, madzi
Woyipayo atsikira konko
Oh palibe
Palibe alibe mavuto
Ali wa moyo pa dziko lapansi
Oh ndi iyeyo
Ndiyekhayo womwalira
Wathana nazo zapadziko
Muli nchisimu choweluza
Awa ngoyina inu ngabwino
Mumayiwala munthu aliyense
Ali ndi zake zofooka
Aliyense pa dziko pano
Ali ndi mtanda wake womuzunza
Awo ndi chamba, awo ndi mowa
Awa kunyenga, awa ngotolatola
Tikadzitchula kuti ndife abwino
Tidzinyenga chabe
Tikadziona ndife alunga-lunga
Tingopusa chabe
Poti wabwino ndi Mulungu yekha
Wosachimwa kose
Mavuto onse tipereke kwa iye
Mbuye wotilenga
Palibe munthu wopanda tchimo
Dziko lapansi ndi lochimwa
Adatitsoka mtunda, madzi
Woyipayo atsikira konko
Palibe alibe mavuto
Ali wa moyo pa dziko lapansi
Ndiyekhayo womwalira
Wathana nazo zapadziko
Pali kagulu ka anthu ena
Amakonda kunyogodola
Akawona nzawo akuvutika
Samathandiza awo m'manong'onong'o
Aliyense padzikopa inu
Ali ndi nthenda yomwe idzamuzunze
Ena ndi sugar, BP, asthma
Khunyu, edzi ena adzalumala
Tikadzitchula kuti ndife abwino
Tidzinyenga chabe
Tikadziona ndife alunga-lunga
Tingopusa chabe
Poti wabwino ndi Mulungu yekha
Wosachimwa kose
Mavuto onse tipereke kwa iye
Mbuye wotilenga
Palibe munthu wopanda tchimo
Dziko lapansi ndi lochimwa
Adatitsoka mtunda, madzi
Woyipayo atsikira konko
Palibe alibe mavuto
Ali wa moyo pa dziko lapansi
Ndiyekhayo womwalira
Wathana nazo zapadziko

Palibe munthu wopanda tchimo
Dziko lapansi ndi lochimwa
Adatitsoka mtunda, madzi
Woyipayo atsikira konko
Oh palibe, palibe alibe mavuto
Ali wa moyo pa dziko lapansi
Oh ndi iyeyo
Ndiyekhayo womwalira
Wathana nazo zapadziko
Palibe munthu wopanda tchimo
Dziko lapansi ndi lochimwa
Adatitsoka mtunda, madzi
Woyipayo atsikira konko
Palibe alibe mavuto
(Ali wa moyo pa dziko lapansi)
(Ndiyekhayo womwalira)

Поcмотреть все песни артиста

Other albums by the artist

Similar artists