Kishore Kumar Hits

Lucius Banda - Angoni / Mabala / Samuel / Tina / Esther / Nthawi / Sijacuzi / Paulendo / Mzimu Wa Soldier / Yell lyrics

Artist: Lucius Banda

album: Angoni / Mabala / Samuel / Tina / Esther / Nthawi / Sijacuzi / Paulendo / Mzimu Wa Soldier / Yell


Angoni ndikakwatira
Mudzandiphere chi Kuzi
Nzatchinjirize uwende
Muzawutsire tsabola
Oh Angoni
Oh Angoni
Koma kuti chingoni chikome
Msadzalephere ka mbiya
Kachipanda wa masese
Koma lawi lawi ukuwira
Oh Angoni
Koma oh Angoni
Ngodya za Angoni ndi zingati lero?
Ngodya zathu ndi zinayi
Ngodya za Angoni ndi zingati lero?
Ngodya zathu ndi zinayi
Nyama, mowa, ngoma
Kamkazi kali pambalipa
Koyimba nthungululu
Yi hi
Kunali anthu ena ongovutika
M'mene anthu ena amkangokondwela
Panali anthu ena ongogwira ntchito
Pamene anthu ena amkangodyelera
Malume ndalama kubisa ku bank
Pamene mbumba yanu ikufa ndi njala
Koma zowuluka zonse zitawuluka, pali tsiku limodzi zitadzatele
Inu mumati zidzakhala choncho
Mpaka liti abale?
Ana a Mulungu sangakhare akulira ma days onse a moyo wawo
Analanda ufumu kalero
Nawupeleka kwa woyenera
Ndipo ndichani chingamulake
Mbuye Mulungu wachilungamo, (ah oh oh)
Ndi wachikondi
Mwana ngati ine, Samuel Samuel anathananga mwana
Kupita kwa Eli mwandiyitana ine
Kufika kwa Eli, anamka na Eli
Ati pita ukagone
Sin'nakuyitane ine
Ambuye wayitana, usakane iwe
Utsegule mtima alowemo iye
Ambuye wakutuma, usathawe iwe
Kungatalike ukalarike iwe, (ndamva za Samuel ndimve za Tina)
Iwe Tina tabwela, (ooh)
Ndili ndi ti mawu, (mmh)
Ndikupita ku Lilongwe
Kukafuna ntchito
Undipatse chala Tina
Ndiyikeko mphete
Kuti ikhale chikole
Cha chikondi changa
Ndiwe okongola
Ndiwe okongola Tina
Ndiwe okongola
Undidikilire
Wakusalala
Perfume wa wecheweche
Ndiwe wokongola
Undidikilire
Love of my life Ester
Ndizavale bwanji kuti uzandindikonde
Love of my life Ester
Ndidzavale bwanji kuti udzandikonde
Andipatsa phuma a tidye nawo
Pitani kuyali nauchopi
Inu a ogodi akhaza
Lero ndagoma ndapaya
Ndinali ndekha pa dzana
Nditafunda ntchetche ngati Yobe
Kuchipanda abale anga
Ndinali yani ine?
Lero mwandizungulira ine
Mowa mufuna nzigula
Koma dzana ndi dzulo lija
Lidali sorry site
Panalibe m'modzi yemwe
Okumbukira dzina langa
Munanditaya atsamunda
Kusiyira mkazi mwana
Oh nthawi yandiphuzitsa chiphuziro
Nthawi yandionetsa zinthu
Abwenzi ndingathe kuwaloza ine
Nthawi yochepa ndatora
Ati nthawi yandiphunzitsa chiphunziro
Nthawi yandionetsa zinthu
Ati abwenzi ndingathe kuwaloza ine
Mu short time ndakula
Iih adayesetsa, kugula zonse
Zofunika, mkazi asangalare
Nyumba ya Jacuzzi
Phone motorola
Ati convertable, mkazi adzinyawuda
Si Jacuzzi, si motorola
Si convertable
Ndikufuna nthawi yako
Sinnakwatire, ndi nyumba yako
Ndalama zako, ndimafuna nthawi yako
Week ndi week, uli mu ndege
Zoti kuli ife, unayiwala
Sindinakwatiwe ndi nyumba yako
Ndalama zako, ndimafuna time yako
Usamavomele, kupondelezedwa
Sampatse movuta
Poti moyo lero ndi pokokera pako
Vara zilimbe iwe
Anzako ambiri anagwa panjira
Iwe walimba tu
Takokera mphamvu, dzuka ndi ulendo
Paulendo, paulendo
Ukagwa udzuke udzisase matope
Tikafike ku Kenani
Koma paulendo
Koma paulendo
Ukagwa udzuke udzisase matope
Tiwoloke Yolodano
Ine ndikhumba, Mbuye Yesu
Mudzakhale pompo mkamadzafa
Ndikamasimba za imfa yanga
Abwenzi ambiri samakondwa
Koma ndithu tonsefe tidzafa
Ngati si mawa koma mkuja
Koma ndithudi pa maliro panga
Msadzachulutse zotokota
Nzimu wanga udzakondwa, (powona kuti)
Aphawi amasiye, (anzawo awalandira)
Abale anga osawukawa, (mukuwaganizira?)
Aphawi, amaziye, (aphunzire zimodzi)
Nzimu wa Soldier udzagona
Nzimu wa Soldier udzagona
Nzimu wa Namadingo udzagona
Nzimu wa soldier udzagona
Koma mundilore, (ukuti bwanji?)
Kuti ndisanamalize, (uh huh)
Ndiyimbe ya pa mtima panga, (imba mphwanga iwe)
Oh oh oh oh oh yeah yeah
Angakhale ufune usafune
U ih uh uh chisankho idawina
Nnazungulira dziko la Malawi
Aliyese nkhani ndi ya iwowo
Ndayenda uh!
Ndi a Chair waliwali
Mudayenda uh! ndi a Bingu waliwali
Namadingo mvetsera mawu anga, (ndili chete kumvetsera)
Moyo uno wasintha, palibeso chabwino
Ngakhale nyeno ndiyopenga
Mvulayi ingogwa nthawi yakeyake
Kunali mawungu ndi misale
Tinali wokondwa kwa chaka chonse ife
Mbewu za kumunda zimkalora
Opanda feteleza moyo unali wabwino woh ooh
Pano lili kuti nzanga dziko lija
Pomwe ana amkangolira poti ndi wana osati njala
Lili kuti lili kuti nzanga dziko lija ah
Pomwe mphongo zimkangothawa
Kuthawa njoka osati munthu
Ukanangophinya diso
Ukanangondinong'oneza
Ukanandikanda m'maja
Sindimkadziwa umandifuna
Namadingo usawope mkazi akatchena, (ine nde sindiopa)
Kutchenaku amafuna inu mumukonde
Angakongole bwanji
Akusowa chikondi cha bambo
Angalemere bwanji, amachisowa cha abambo
Chikondi ih ih, tikunena chikondi cha bambo
Amayi ih ih ih
Abambo oh
Musaope mkazi mkazi akatchena
Tsitsi lawo ndi chipewa amatha kuvula

Поcмотреть все песни артиста

Other albums by the artist

Similar artists