Nthawi tigwa m'mavuto
Ndiyo nthawi ya choona
Imene munthu aliyense amathawira kodalira
Awa anzathu achuma amadalira chuma chawo
Nawo anzathu okhwimawo amadalira nyanga zawo
Musamagwade pansi kupempha dzovala mchakudya
Mbalame m'nyama za ntchire kodi zikhala moyo bwanji?
Amaveka maluwa namadyetsa amisala
Gome la ufumu wake poti zonse uzazipeza
Ndililabe, ndililabe kwa Inu Mbuye wanga
Ndililabe, ndililabe kwa Inu Mlengi wanga
Chuma changa, zanga zonse ndi unu Mbuye wanga
Ndikakondwa, ndikalira nditsamira kwa Inu

Ndinalila, ndilindila kwa Inu Mlengi wanga
Chuma changa, zanga zonse ndi Inu Mbuye wanga

♪
Pomwe njala yavuta usiwale ntakutuluza
Sukulu adabwelera mkazi wako akudwala
Ntchito yako yatha angongole afuna zawo
Satana ndiye akondwa kufuna kuona mphamvu zako
Kumbukira Yobo ndiye oyamba kuzuzika
Mkazi wake amene akuti Yobo nyoza Mbuye
Koma ngati uli wake mpamene udzadziwe choona
Tsamira Mbuye Mulungu pakuti ndiye mpulumutsi
Ndililabe, ndililabe kwa Inu Mbuye wanga
Ndililabe, ndililabe kwa Inu Mlengi wanga
Chuma changa, zanga zonse ndi Inu Mbuye wanga
Ndikakondwa, ndikalira nditsamira kwa Inu
Ndililabe, ndililabe kwa Inu Mbuye wanga
Ndinalila, ndilindila kwa Inu Mlengi wanga
Chuma changa, zanga zonse ndi unu Mbuye wanga
Ndikakondwa, ndikalira nditsamira kwa Inu
Monga mwana wakhandayo
Nthawi ya nkuthompha dziwa
Kukakamira ku bere la mayi wake
Nawe m'bale wa Yesu yo
Nthawi iyo yachinyengo
Mchititse nyazi Satana kwa Mbuye wako
Ndililabe, ndililabe kwa Inu Mbuye wanga
Ndililabe, ndililabe kwa Inu Mlengi wanga
Chuma changa, zanga zonse ndi Inu Mbuye wanga
Ndikakondwa, ndikalira nditsamira kwa Inu
Ndililabe, ndililabe kwa Inu Mbuye wanga
Ndinalila, ndilindila kwa Inu Mlengi wanga
Chuma changa, zanga zonse ndi Inu Mbuye wanga
Ndikakondwa, ndikalira nditsamira kwa Inu
Поcмотреть все песни артиста
Other albums by the artist