Mimba yake bambo ake anayika
Sindifunaso mwana ine uyu yekha mukachotsetse
Mayi wake ndi chikondi nakakakamira
Mpaka banja linatha anabadwa mkukula movutikira
Mpaka tsiku lina mwana atafooka ndi njala
Adakaba ku maliro, nsima ndi ndiwo
Mpaka tsiku lina mwana fees itasowa
Adapita pa hotel uhule mwana aphunzire
Oooh why?
Akanadziwa mayi mayiyo
Mwana ali m'mimbayo akadzabadwa
Adzawanyoza, adzawakana akanamutani?
Akanadziwa nzakeyo
Bwezi ndikuthandiza zikayenda
Adzamutaya, adzamunyoza akanamutani?
Chosadziwa, chosadziwa
Chosadziwa, zimangochitika
Namalenga, amaona
Ndalakwanji? zimangochitika
Oooh why?
Waphunzira mkumaliza lero walemera
Wayambapo kunyoza mayi mumkaba komanso uhule
Akabwera ku town akumawazemba
Dziko likudabwa ndiwe munthu wanji
Kodi wayiwala?
Ulavure nsimayo poti inali yakuba
Ung'ambe degree poti fees ya uhule
Waliputa tsoka ona njala yavuta
Chaka ndiye chatha popanda chochita
Oooh why?
Eh yeah, eh yeah, eh yeah
Akanadziwa mayi mayiyo
Mwana ali m'mimbayo akadzabadwa
Adzawanyoza, adzawakana akanamutani?
Akanadziwa nzakeyo
Bwezi akuthandiza zikayenda
Adzamutaya, adzamunyoza akanamutani?
Chosadziwa, chosadziwa
Chosadziwa, zimangochitika
Namalenga, amaona
Talakwanji? mukhululuke
Kundidabwitsa dyamani anthu amakono
Kutembenuka poyela kutukwana mayi kufuna mipando
Amkaphuzitsa ku Madalasi ku Mpemba
Anali ma nobody awatsukatsuka kumalalata
Zoonadi ndalama inapha Yesu
Ndimadina dance
Ma phwando a wisiki
Mudzatikumbukira kunja kukacha
Tinkakoma mu dzinja, mchilimwe tanyasa
Yeah hii why?
Akanadziwa mayi mayiyo
Mwana ali m'mimbamu akadzabadwa
Adzawanyoza, adzawakana akanamutani?
Akanadziwa nzakeyo
Bwezi ndikuthandiza zikayenda
Adzamutaya, adzamunyoza akanamutani?
Chosadziwa, chosadziwa
Chosadziwa, zimangochitika
Namalenga, amaona
Talakwanji? mukhululuke
Oooh why?
Chosadziwa, chosadziwa
Chosadziwa, zimangochitika
Namalenga, amaona
(Talakwanji? mukhululuke)
Поcмотреть все песни артиста
Other albums by the artist