Kishore Kumar Hits

Lucius Banda - Kapitao lyrics

Artist: Lucius Banda

album: Money and Power


Let us remember to be grateful to God
For keeping us alive
Akapitao nkhanza
Ana sankanena kanthu
Ana sanali woyipa
Mumkangotseka ndinu
Anali adokotala oyesetsa kusamala mbumba
Adafa mbiri yachabe
Wolakwa Akapitao
Let us also not forget that God
Chisoni Agadama
Chikweza pumanayeni
Agogo amkamukonda
Koma Kapitao zimkamunyasa
Momwe adathera athu
Agogo asakudziwa
Amkamva zotha itha
Kapitao amkapha anthu
Ngati ankazunza anthu ali nduna uyo
Kodi adzazunza bwanji akafikapo?
Amkakondera akwawo ali wamba uyo
Kodi ena tidzatani akafikapo?
Milandu yonse amkawina olo alakwe uyo
Kodi adzawina bwanji akalowa m'boma?
Akwathu nthenda yathu ndi kuyiwala inu
Komatu m'makumbuka tinavutika
Do not forget that God the almighty father
Has given us many other blessings
In the course of the past years
Ali ndi magazi m'manja
Yekhayo chonde mtayeni
Ndi danger mukugwirayo
Mukuyatsa moto wa petulo
Tukwana nzimu kumanda
Ambiri anatisiya
Wosalakwa ali mu shire
Adawapha pofuna mpando

Agogo amkayesetsa
Kuyambitsa zinthu zabwino
Kapitao akazipinda
Mkumapangira nkhanza
Card linalipo bwino
Idali njira yodziwilana
Adayamba kutsekela nsika
Sukulu ndi chipatala
Ngati ankazunza anthu ali nduna uyo
Kodi adzazunza bwanji akafikapo?
Amkakondera akwawo ali wamba uyo
Kodi ena tidzatani akafikapo?
Milandu yonse amkawina olo alakwe uyo
Kodi adzawina bwanji akalowa m'boma?
Akwathu nthenda yathu nkuyiwala inu
Komatu m'makumbuka tinavutika

Tithokoze bwana Muluzi
Wathetsa nkhanza zonsezi
Kukhala kupusa kwathu
Kubwenzelaso nkhanza
1964 adalipo mu parliament
Lero adakaliso phungu
Kodi mudzapuma liti?
Amalawi tatopa nanu
Muleke tione zina
Mulore Bingu alowe
Tione za mtundu wina
Bingu ndi munthu ofatsa
Wopanda mbiri zakupha
Maphunziro ndi okwana
Tiyeni tione zina
Ngati anazunza anthu ali nduna uyo
Kodi adzazunza bwanji akafikapo?
Amkakondera akwawo ali wamba uyo
Kodi ena tidzatani akafikapo?
Milandu yonse amkawina olo alakwe uyo
Kodi adzawina bwanji akalowa m'boma?
Akwathu nthenda yathu ndi kuyiwala inu
Komatu m'makumbuka tidavutika
Let us also not forget that God the almighty father
Has given us many other blessings
In the course of the past years
Therefore i wish you all my people
A very very happy and prosperous new year
Ngati anazunza anthu ali nduna uyo
Kodi adzazunza bwanji akafikapo?
Amkakondera akwawo ali wamba uyo
Kodi ena tidzatani akafikapo?
Milandu yonse amkawina olo alakwe uyo
Kodi adzawina bwanji akalowa m'boma?
(Akwathu nthenda yathu ndi kuyiwala inu)
(Komatu m'makumbuka tidavutika)

Поcмотреть все песни артиста

Other albums by the artist

Similar artists