Kishore Kumar Hits

Lucius Banda - Ndisiyireni Kanga lyrics

Artist: Lucius Banda

album: Fifteen Fifteen


Oh oh oh oh
Oh no no, oh no no
Oh ooh
Mukati mutchene ma label bwana
Perfume ndi hugo boss
Galimoto ya mtundu wa hummer
Nyumba yanu ngati reserve bank
Mkazi aliyese amasilira
Olo atakhala mkazi wachitatu, chilichose azizipangira
Bola azitchedwa akazi anu
Koma chomwe chidabwitsa
Kusiya ulemelero wonsewo
Kubwela kuno kwa Che Musa
Kuzandilanda wangayu
Oh ooh ooh, no
Ndisiyireni kanga
Ndi komwe ndili nako ine
Ndikomwe mbuye anandipatsa
Ndisiyireni bwana
Ine ndilibe hummer, ngakhale tv ndilibe ine
Mwa iyeyo ndipeza zonse
Ndisiyireni bwana
Usakhale ngati mfumu David
Inali ndi chuma chambirimbiri
Kubwela mlendo, kupanda chifundo
Kukapha ka nkhosa ka mphawiyo
Muli ndi chuma chambirimbiri
Ma lorry, ma bus ndi zigayo
Ife timkadyero wokala yomweyo
Mwazamangapo grocery
Koma chomwe chidabwitsa
Kusiya chuma chonsecho
Kubwela kuno kwa Mayaka
Kudzaphangira amphawi
Oh ooh ooh
Ndisiyireni kanga
Ndi komwe ndili nako ine
Ndikomwe mbuye anandipatsa
Ndisiyireni bwana
Ine ndilibe hummer, ngakhale tv ndilibe ine
Mwa iyeyo ndipeza zonse
Ndisiyireni bwana
Ndisiyireni kanga
Ndi komwe ndili nako ine
Ndikomwe mbuye anandipatsa
Ndisiyireni bwana
Ine ndilibe hummer, ngakhale tv ndilibe ine
Mwa iyeyo ndipeza zonse
Ndisiyireni bwana
Iwe mkazi wanga usatengeke
Gwero la chuma chawo sukulidziwa
Mwina ndi zakuba, zophera anthu
Uzangosandutsidwako ndondocha
Ali ndi ngongole zambirimbiri
Kuti agone amamwa barium
Amaoneka wolemera kunjaku
Mumtima mwawo mulitu umphawi
Timadya bonongwe mosangalala
Osati nkhuku zawo za tcheu tcheu
Mtendere wamumtima uposa zose
Nthawi yathuso izafika
Bwera mkazi wanga tsono tivine
Tinyadire, tithokoze Mulungu
Ali ndi cholinga pokutilenga
Ona ma bwana akukusilira
Mwamuna uja mudataya
Lero ndi phungu wachuma
Chikhwaya chija mutsata
Chidalowa pagalaputi
Oh ooh ooh, no oh
Ndisiyireni kanga, (ayi ayi ayi ayi)
Ndi komwe ndili nako ine, (oh oh oh)
Ndikomwe mbuye anandipatsa, (oh oh oh)
Ndisiyireni bwana
Hummer ndilibe ine, ine ndilibe hummer
Tv ndilibe ine,ngakhale tv ndilibe ine, (ooh oh)
Mwa iyeyo ndipeza zonse. (ooh oh)
Ndisiyireni bwana
Ndisiyireni, ndisiyireni kanga
Ndisiyireni, ndi komwe ndili nako ine, (oh oh oh)
Ndikomwe mbuye anandipatsa, (oh oh oh)
Ndisiyireni bwana
Hummer ndilibe ine, ine ndilibe hummer
Tv ndilibe ine,ngakhale tv ndilibe ine, (ooh oh)
Mwa iyeyo ndipeza zonse. (ooh oh)
Ndisiyireni bwana

Поcмотреть все песни артиста

Other albums by the artist

Similar artists